AHEBRI 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Khristu Mwana wa Mulungu aposatu angelo

1Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,

2Mat. 21.38; Yoh. 1.17koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;

3Yoh. 1.4, 14; Aheb. 7.27; Aef. 1.20ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,

4Afi. 2.9-10atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.

5Mas. 2.7; 2Sam. 7.14Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse,

Iwe ndiwe Mwana wanga,

lero Ine ndakubala Iwe?

Ndiponso,

Ine ndidzakhala kwa Iye Atate,

ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?

6 Aro. 8.29; 1Pet. 3.22 Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.

7 Mas. 104.4 Ndipo za angelo anenadi,

Amene ayesa angelo ake mizimu,

ndi omtumikira Iye akhale malawi amoto.

8 Mas. 45.6-7 Koma ponena za Mwana, ati,

Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;

ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

9 Yes. 61.1 Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa;

mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani

ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.

10 Mas. 102.25-27 Ndipo,

Inu, Ambuye, pachiyambipo munaika maziko ake a dziko,

ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu.

11Iyo idzataika; komatu mukhalitsa;

ndipo iyo yonse idzasuka monga malaya;

12ndi monga chofunda mudzaipinda

monga malaya, ndipo idzasanduka;

koma Inu ndinu yemweyo,

ndipo zaka zanu sizidzatha.

13 Mas. 110.1 Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?

14 Mas. 34.7; Mac. 27.25 Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help