EZEKIELE 32 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nyimbo ya maliro ya pa Farao

1Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri, mwezi wakhumi ndi chiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

2Ezk. 29.3; Yer. 46.8Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.

3Hos. 7.12Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga.

4Ezk. 31.13Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zilombo za dziko lonse lapansi ndi iwe.

5Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako.

6Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe.

7Yes. 13.10; Yow. 2.31; Mat. 24.29Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.

8Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuunikira kuthambo, ndi kuchititsa mdima padziko lako, ati Ambuye Yehova.

9Ndidzavutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine chionongeko chako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwe.

10Ezk. 27.35Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzachita malunga chifukwa cha iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense chifukwa cha moyo wake tsiku lakugwa iwe.

11Yer. 46.25-26Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babiloni lidzakudzera.

12Ezk. 28.7Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Ejipito, ndi aunyinji ake onse adzaonongeka.

13Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira.

14Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ake, ndi kuyendetsa madzi a m'mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova.

15Eks. 7.5Pakusanduliza Ine dziko la Ejipito likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zake, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

162Mbi. 35.25Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.

Mau a kulirira aunyinji a Ejipito

17Kunalinso chaka chakhumi ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,

18Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana aakazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

19Ezk. 31.18Uposa yani m'kukoma kwako? Tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.

20Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ake onse.

21Ezk. 32.19-25Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ake, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga.

22Ezk. 32.24, 26, 29-30Asiriya ali komwe ndi msonkhano wake wonse, manda ake amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;

23Ezk. 32.24, 26, 29-30manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lake lizinga manda ake; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anopsetsa m'dziko la amoyo.

24Ezk. 32.24, 26, 29-30Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

25Ezk. 32.24, 26, 29-30Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ake onse, manda ake amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa.

26Ezk. 32.24, 26, 29-30Meseki, Tubala, ndi aunyinji ake onse ali komweko, manda ake amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.

27Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao zili pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.

28Ndipo udzathyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.

29Edomu ali komwe, mafumu ake ndi akalonga ake onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.

30Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Asidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nachita manyazi chifukwa cha kuopsetsa anachititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.

31Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ake onse, Farao ndi ankhondo ake onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

32Pakuti ndinaika kuopsa kwake m'dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help