MLALIKI 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za m'moyo uno sizitha kukondweretsa mtima

1 Luk. 12.19 Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.

2Miy. 14.13Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?

3Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

4Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;

5ndinakonza mphanje ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundumitundu;

6ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo;

7ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine;

81Maf. 9.28ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.

9Mlal. 1.16Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.

10Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli.

11Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

12Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.

13Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

14Miy. 17.24Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.

15Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.

16Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.

17Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

18Mas. 49.10Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata.

19Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.

20Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.

21Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.

22Pakuti munthu ali ndi chiyani m'ntchito zake zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?

23Yob. 5.7Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe.

24Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.

25Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.

26Yob. 27.16-17Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help