1 SAMUELE 21 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide athawira kwa wansembe Ahimeleki ku Nobu

1Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?

2Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.

3Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho.

4Lev. 24.5-9; Mat. 12.3-4Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.

5Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; chichokere ine, zotengera za anyamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wachabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?

6Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.

71Sam. 22.9Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo.

8Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.

91Sam. 17.51Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.

Davide athawira kwa Akisi

10Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.

111Sam. 18.7Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti,

Saulo anapha zikwi zake,

koma Davide zikwi zake zankhani?

12Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.

13Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.

14Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji?

15Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help