NYIMBO YA SOLOMONI 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mas. 36.8 Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi:

Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga;

ndadya uchi wanga ndi chisa chake;

ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.

Idyani, atsamwalinu,

imwani, mwetsani chikondi.

Alekana nthawi

2 Chiv. 3.20; Yoh. 3.29 Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso:

Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati,

nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga,

nkhunda yanga, wangwiro wanga.

Pakuti pamutu panga padzala mame,

patsitsi panga pali madontho a usiku.

3Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji?

Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenji?

4Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera,

mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye.

5Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;

pamanja panga panakha mure.

Ndi pa zala zanga madzi a mure,

pa zogwirira za mpikizo.

6Ndinamtsegulira bwenzi langalo;

koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka.

Moyo wanga unalefuka polankhula iye:

Ndinamfunafuna, osampeza;

ndinamuitana, koma sanandivomere.

7Alonda akuyenda m'mzinda anandipeza,

nandikantha, nanditema;

osunga makoma nandichotsera chophimba changa.

8Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu,

mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani?

Kuti ndadwala ndi chikondi.

9Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,

mkaziwe woposa kukongola?

Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,

kuti utilumbirira motero?

10 Mas. 45.2; Yoh. 1.14 Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,

womveka mwa zikwi khumi.

11Mutu wake ukunga golide, woyengetsa,

tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khwangwala.

12Ana a maso ake akunga nkhunda

pambali pa mitsinje ya madzi;

otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.

13Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo,

ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:

Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.

14Manja ake akunga zing'anda zagolide

zoikamo zonyezimira zoti biriwiri.

Thupi lake likunga chopanga cha minyanga

cholemberapo masafiro.

15Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,

zogwirika m'kamwa mwa golide:

Maonekedwe ake akunga Lebanoni,

okometsetsa ngati mikungudza.

16M'kamwa mwake muli mokoma; inde,

ndiye wokondweretsa ndithu.

Ameneyu ndi wokondedwa wanga,

ameneyu ndi bwenzi langa,

ana aakazi inu a ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help