1Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,
ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 Yes. 11.2-4 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo,
ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo.
3 Yes. 52.7 Mapiri adzatengera anthu mtendere,
timapiri tomwe, m'chilungamo.
4Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,
adzapulumutsa ana aumphawi,
nadzaphwanya wosautsa.
5 Mas. 89.36-37 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,
kufikira mibadwomibadwo.
6 Hos. 6.3 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga,
monga mvula yothirira dziko.
7 Yes. 2.4 Masiku ake wolungama adzakhazikika;
ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.
8 1Maf. 4.21, 24; Zek. 9.10 Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja,
ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.
9 Yes. 49.23 Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake;
ndi adani ake adzaluma nthaka.
10 Yes. 60.6, 9 Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka;
mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.
11 Yes. 49.22-23 Inde mafumu onse adzamgwadira iye,
amitundu onse adzamtumikira.
12 Mas. 35.10 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo;
ndi wozunzika amene alibe mthandizi.
13Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi,
nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.
14 Mas. 116.15 Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa;
ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.
15Ndipo iye adzakhala ndi moyo;
ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba;
nadzampempherera kosalekeza;
adzamlemekeza tsiku lonse.
16M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka
pamwamba pa mapiri;
zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni,
ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.
17 Gen. 22.18; Mas. 89.36 Dzina lake lidzakhala kosatha,
momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu.
Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;
amitundu onse adzamutcha wodala.
18 Mas. 77.14 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele,
amene achita zodabwitsa yekhayo.
19 Neh. 9.5; Zek. 14.9 Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha;
ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake.
Amen, ndi Amen.
20Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.