1 Mas. 18.1 Ndimkonda, popeza Yehova amamva
mau anga ndi kupemba kwanga.
2Popeza amanditcherera khutu lake,
chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse.
3 Mas. 18.4-6 Zingwe za imfa zinandizinga,
ndi zowawa za manda zinandigwira:
ndinapeza nsautso ndi chisoni.
4Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova;
ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
5 Mas. 103.8 Yehova ngwa chifundo ndi wolungama;
ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.
6Yehova asunga opusa;
ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.
7 Mat. 11.29 Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako;
pakuti Yehova anakuchitira chokoma.
8 Mas. 56.13 Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa,
maso anga kumisozi,
mapazi anga, ndingagwe.
9Ndidzayenda pamaso pa Yehova
m'dziko la amoyo.
10 2Ako. 4.13 Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula;
ndinazunzika kwambiri.
11 Aro. 3.4 Pofulumizidwa mtima ndinati ine,
anthu onse nga mabodza.
12Ndidzabwezera Yehova chiyani
chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?
13Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso,
ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.
14 Mac. 18.18 Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,
tsopano, pamaso pa anthu ake onse.
15 Mas. 72.14 Imfa ya okondedwa ake
nja mtengo wake pamaso pa Yehova.
16 Mas. 119.125 Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu;
ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
mwandimasulira zondimanga.
17 Lev. 7.12; Mas. 50.14 Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko,
ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.
18 Mas. 116.14 Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova,
tsopano, pamaso pa anthu ake onse.
19 Mas. 135.2-3 M'mabwalo a nyumba ya Yehova,
pakati pa inu, Yerusalemu.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.