MASALIMO 145 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ukulu ndi ukoma wa MulunguSalimo lolemekeza; la Davide.

1Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;

ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

2Masiku onse ndidzakuyamikani;

ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

3 Mas. 96.4; Aro. 11.33 Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ndi ukulu wake ngwosasanthulika.

4 Yes. 38.19 Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake,

ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

5Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu,

ndi ntchito zanu zodabwitsa.

6Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa;

ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu,

nadzaimbira chilungamo chanu.

8 Eks. 34.6-7 Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo;

osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.

9 Mlal. 12.7 Yehova achitira chokoma onse;

ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

10 Mas. 19.1 Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;

ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,

adzalankhulira mphamvu yanu.

12Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake,

ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.

13 1Tim. 1.17 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,

ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.

14Yehova agwiriziza onse akugwa,

naongoletsa onse owerama.

15 Mas. 104.27-28; 136.25 Maso a onse ayembekeza Inu;

ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.

16 Mas. 147.9 Muolowetsa dzanja lanu,

nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

17Yehova ali wolungama m'njira zake zonse,

ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.

18 Deut. 4.7; Mas. 119.151; Yoh. 4.24 Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,

onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

19Adzachita chokhumba iwo akumuopa;

nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

20 Mas. 31.22-23 Yehova asunga onse akukondana naye;

koma oipa onse adzawaononga.

21Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova;

ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera

kunthawi za nthawi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help