1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.
3Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele.
4Maina ao ndi awa: wa fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri.
5Wa fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori.
6Wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.
7Wa fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe.
8Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni.
9Wa fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu.
10Wa fuko la Zebuloni, Gadiele mwana wa Sodi.
11Wa fuko la Yosefe, wa fuko la Manase, Gadi mwana wa Susi.
12Wa fuko la Dani, Amiyele mwana wa Gemali.
13Wa fuko la Asere, Seturi mwana wa Mikaele.
14Wa fuko la Nafutali, Nabi mwana wa Vofusi.
15Wa fuko la Gadi, Geuwele mwana wa Maki.
16Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
17Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwera, nimukwere kumapiri;
18mukaone dziko umo liliri; ndi anthu akukhala m'mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofooka, ngati achepa kapena achuluka;
19ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri mizindayo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga;
20ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.
21Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.
22Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)
23Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.
24Malowa anawatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsangolo ana a Israele analichekako.
25Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.
26Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
27Eks. 3.8Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.
28Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.
29Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.
30Num. 14.6; Yos. 14.7Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.
31Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitingathe kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu.
32Num. 14.36Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu.
33Yes. 40.22Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.