DEUTERONOMO 18 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zoyenera ansembe ndi Alevi

1 Num. 18 Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.

2Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.

3Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu.

4Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.

5Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao aamuna kosalekeza.

6Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;

7pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.

8Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.

Mulungu aipidwa nao anyanga ndi obwebweta ndi onse otere

9 Lev. 18.21-24 Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.

10Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.

11Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.

12Deut. 9.4Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

13Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.

14Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.

Lonjezo lakuti adzabadwa mneneri womveka

15 Yoh. 1.21, 45; Mac. 3.22; 7.37 Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;

16Eks. 20.19monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu mu Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.

17Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi.

18Deut. 18.15Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.

19Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.

20Yer. 14.14Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.

21Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?

22Yer. 28.9Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help