1Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,
2Yer. 37.3-10Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.
3Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:
4Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.
5Eks. 6.6Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi mu ukali waukulu.
6Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mzinda uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi mliri waukulu.
7Yer. 37.17Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.
8Deut. 30.19Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.
9Yer. 38.2-3, 17-18Iye amene akhala m'mzinda uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.
10Mas. 34.16; Yer. 38.2-3, 17-18Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.
Aneneratu motsutsa mbumba yachifumu ya Yuda11Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:
12Zek. 7.9Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.
13Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?
14Miy. 1.31; Yes. 3.10-11Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.