OWERUZA 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Efuremu aukira Yefita

1Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamutu pako.

2Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutse m'dzanja lao.

31Sam. 19.5Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo?

41Sam. 25.10; Mas. 78.9Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a mu Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase.

5Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai;

6pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.

7Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mzinda wina wa Giliyadi.

Oweruza Ibzani, Eloni, Abidoni

8Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele.

9Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu; ndi ana aakazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake aamuna ana aakazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri.

10Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu.

11Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi.

12Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa mu Ayaloni m'dziko la Zebuloni.

13Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele.

14Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.

15Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa mu Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help