1Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti,
2Yos. 14.3-4; Ezk. 45.1Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, mizinda yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira mizinda.
3Ndipo mizinda ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse.
4Ndipo mabusa a mizindayo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.
5Ndipo muyese kunja kwa mzinda, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mzindawo pakati; ndiwo mabusa a kumizinda.
6Yos. 20.2, 7-8Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.
7 Yos. 21.41 Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao.
8Ndipo kunena za mizindayo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako mizinda yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
Mizinda yopulumukirako(Deut. 19.1-13; Yos. 20.1-9)9Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
10Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pakuoloka inu Yordani kulowa m'dziko la Kanani,
11muikire mizinda ikukhalireni mizinda yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.
12Deut. 19.6Ndipo mizindayo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.
13Ndipo mizindayo muipereke ikukhalireni mizinda isanu ndi umodzi yopulumukirako.
14Deut. 4.41Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yordani, ndi mizinda itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako.
15Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.
16Eks. 21.12, 14Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
17Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
18Kapena akamkantha m'dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
19Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.
20Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;
21kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.
22Eks. 21.13Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira,
23kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wake, kapena womfunira choipa;
24pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;
25ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.
26Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mzinda wake wopulumukirako kumene anathawirako;
27nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;
28popeza wakupha munthu akadakhala m'mzinda wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.
29Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.
30Deut. 17.6; Mat. 18.16; 2Ako. 13.1; Aheb. 10.28Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.
31Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.
32Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumzinda wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.
33Gen. 9.6Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.
34Eks. 29.45; Deut. 21.23Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.