1Mwananga, mvera nzeru yanga;
tcherera makutu ku luntha langa;
2ukasunge zolingalira,
milomo yako ilabadire zomwe udziwa.
3 Miy. 2.16; 6.24 Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi;
m'kamwa mwake muti see koposa mafuta.
4Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo,
ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse.
5Mayendedwe ake atsikira kuimfa;
mapazi ake aumirira kumanda;
6sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;
mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye.
7Ndipo tsopano ana, mundimvere,
musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga.
8Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo,
osayandikira ku khomo la nyumba yake;
9kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,
ndi zaka zako kwa ankhanza;
10kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,
ndi kuti usagwire ntchito m'nyumba ya wachilendo;
11ungalire pa chimaliziro chako,
pothera nyama yako ndi thupi lako;
12ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,
mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo;
13ndipo sindinamvere mau a aphunzitsi anga;
ngakhale kutcherera makutu kwa akundilanga mwambo!
14Ndikadakhala m'zoipa zonse,
m'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.
15Imwa madzi a m'chitsime mwako,
ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.
16Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,
ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?
17Ikhale ya iwe wekha,
si ya alendo okhala nawe ai.
18Adalitsike kasupe wako;
ukondwere ndi mkazi wokula nayo.
19Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo,
maere ake akukwanire nthawi zonse;
ukodwe ndi chikondi chake osaleka.
20Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere,
ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?
21 Yer. 16.17; Hos. 7.2 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,
asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.
22 Mas. 9.15 Zoipa zakezake zidzagwira woipa;
adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.
23Adzafa posowa mwambo;
adzasochera popusa kwambiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.