1 MBIRI 16 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 2Sam. 6.17-19 Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, naliika pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.

2Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.

3Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma.

4Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele.

5Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;

6ndi Benaya ndi Yahaziele ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la chipangano la Mulungu.

Salimo la Davide(Mas. 105.1-15; 96.1-13; 106.1, 47-48)

7Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ochita ndiwo Asafu ndi abale ake.

8 2Sam. 23.1; Mas. 105.1-15 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;

bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye.

9Muimbireni, muimbireni zomlemekeza;

fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

10Mudzitamandire ndi dzina lake lopatulika;

mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.

11Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake;

funani nkhope yake nthawi zonse.

12Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita,

zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.

13Inu mbeu ya Israele mtumiki wake,

inu ana a Yakobo, osankhika ake.

14Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;

maweruzo ake akhala padziko lonse lapansi.

15Kumbukirani chipangano chake kosatha,

mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

16 Gen. 17.2; 26.3; 35.11 chipanganocho anapangana ndi Abrahamu,

ndi lumbiro lake ndi Isaki;

17ndipo anachitsimikizira kwa Yakobo chikhale malemba,

chikhale chipangano chosatha kwa Israele;

18ndi kunena kuti,

Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,

gawo la cholowa chako.

19 Deut. 7.7 Pokhala inu anthu owerengeka,

inde anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;

20nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina,

kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena.

21 Eks. 7.15-18 Sanalole munthu awasautse;

ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa;

22ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga,

musamachitira choipa aneneri anga.

23 Mas. 96.1-13 Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi,

lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

24Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu,

zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.

25Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ayenera amuope koposa milungu yonse.

26 Lev. 19.4 Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano;

koma Yehova analenga zakumwamba.

27Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu,

m'malo mwake muli mphamvu ndi chimwemwe.

28Mchitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu,

mchitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

29 Mas. 29.2 Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake;

bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake;

lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.

30Njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi,

dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.

31Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;

anene mwa amitundu, Yehova achita ufumu.

32Nyanja ikukume m'kudzala kwake,

munda ukondwerere, ndi zonse zili m'mwemo.

33Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango

idzafuula mokondwera pamaso pa Yehova;

pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi.

34 Mas. 106.1 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

35 Mas. 106.47-48 Nimunene, Tipulumutseni,

Mulungu wa chipulumutso chathu;

mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu,

kuti tiyamike dzina lanu loyera,

ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.

36Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele,

kuyambira kosayamba kufikira kosatha.

Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova.

37Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;

38ndi Obededomu, ndi abale ake makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obededomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;

391Maf. 3.4ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;

40Eks. 29.38-41kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'chilamulo cha Yehova adachilamulira Israele;

41ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;

42ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata.

43Ndipo anachoka anthu onse, yense kunyumba yake, nabwera Davide kudalitsa nyumba yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help