1 Yoh. 3.32; Chiv. 22.16 Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;
2Chiv. 1.9amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona.
3Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.
Mau a kwa Mipingo isanu ndi iwiri ya mu Asiya4 Eks. 3.14; Zek. 3.9 Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;
5Yoh. 8.14; 1Ako. 15.20; 1Yoh. 1.7ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;
61Pet. 2.5, 9natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
7Mat. 24.30Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.
8 Eks. 3.14; Yes. 41.4; Chiv. 21.6 Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.
Yohane pa chisumbu cha Patimosi. Amlembetsa masomphenya9 Afi. 1.7; Chiv. 6.9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.
10Yoh. 20.26; Mac. 20.7; 1Ako. 16.2Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,
11ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.
12Zek. 4.2; Chiv. 1.20Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;
13Ezk. 1.26ndipo pakati pa zoikaponyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.
14Dan. 7.9Ndipo tsitsi la pamutu pake linali loyera ngati ubweya woyera, ngati chipale chofewa; ndi maso ake ngati lawi la moto;
15Ezk. 43.2ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.
16Mat. 17.2; Aheb. 4.12; Chiv. 1.20Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
17Ezk. 1.28; Chiv. 1.8Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,
18Aro. 6.9ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.
19Chiv. 1.11Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;
20Chiv. 1.12; 2.1chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.