1 Mas. 96.10; Yes. 51.9 Nkokoma kuyamika Yehova,
ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.
2 Mas. 119.147-148 Kuonetsera chifundo chanu mamawa,
ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse.
3 Mas. 33.2 Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa;
pazeze ndi kulira kwake.
4Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu,
ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.
5 Aro. 11.33-34 Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova,
zolingalira zanu nzozama ndithu.
6Munthu wopulukira sachidziwa;
ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;
7 Mas. 37.1-2; 112.10 chakuti pophuka oipa ngati msipu,
ndi popindula ochita zopanda pake;
chitero kuti adzaonongeke kosatha.
8Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.
9 Eks. 15.6 Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,
pakuti, taonani, adani anu adzatayika;
ochita zopanda pake onse adzamwazika.
10 Mas. 23.5 Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;
anandidzoza mafuta atsopano.
11Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira,
m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine
pa iwo akuchita zoipa akundiukira.
12 Mas. 1.3; Hos. 14.5-6 Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;
adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
13Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova,
adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.
14Atakalamba adzapatsanso zipatso;
adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,
15 Deut. 32.4; Aro. 9.14 kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;
Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.