1 YOHANE Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau Oyamba Kalata yoyamba yolembedwa ndi mtumwi Yohane ili ndi mfundo ziwiri zazikulu: mfundo yoyamba ndiyo kulimbikitsa awerengi kuti akhale m'moyo woyanjana ndi Mulungu komanso ndi mwana wake Yesu Khristu, ndipo yachiwiri ndi kuwachenjeza kuti asatsate ziphunzitso zonyenga zimene zikhoza kuononga chiyanjano chao ndi Mulungu. Ziphuzitsozi zimagona pa chikhulupiriro chakuti dziko lapansi ndi loipa ndi munthu amakhala woipa pamene wakhudzana ndi dziko lino. Ankanenanso kuti Yesu amene ali Mwana wa Mulungu, sakadakhala munthu weniweni. Aphunzitsi amenewo amanena kuti munthu akhoza kupulumutsidwa pokhapokha atasiyana kulumikizana ndi dzikoli, komanso amanena kuti chipulumutso sichikhudzana konse ndi khalidwe labwino kapena kukonda anthu ena.Pofuna kutsutsa chiphunzitso chimenechi, wolemba bukuli akunenetsa kuti Yesu Khristu analidi munthu weniweni, ndipo iye akutsindika kuti onse okhulupirira mwa Yesu amakonda Mulungu ndipo ayeneranso kukondana wina ndi mnzake.Za mkatimuMau Oyamba 1.1-4Kuwala ndi mdima 1.5—2.29Ana a Mulungu ndi ana a Satana 3.1-24Choonadi ndi bodza 4.1-6Udindo wa chikondi 4.7-21Chikhulupiriro chopambana 5.1-21