YEREMIYA 47 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aneneratu za chitsutso cha Afilisti

1 Ezk. 25.15-16; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-5 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.

2 Yer. 1.14 Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamzinda ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.

3Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao;

4Yow. 3.4; Amo. 9.7chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.

51Maf. 12.27-29Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?

6Ezk. 21.3-5Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m'chimake; puma, nukhale chete.

7Ezk. 14.17Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m'mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help