1 Mas. 109.1 Mulungu musakhale chete;
musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.
2 Mac. 4.25 Pakuti taonani, adani anu apokosera,
ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.
3Apangana mochenjerera pa anthu anu,
nakhalira upo pa obisika anu.
4 Est. 3.6, 9 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;
ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.
5Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;
anachita chipangano cha pa Inu.
6Mahema a Edomu ndi a Aismaele;
Mowabu ndi Ahagiri;
7Gebala ndi Amoni ndi Amaleke;
Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.
8Asiriya anaphatikana nao;
anakhala dzanja la ana a Loti.
9 Num. 31.7; Ower. 4.15, 24 Muwachitire monga munachitira Midiyani;
ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,
10amene anaonongeka ku Endori;
anakhala ngati ndowe ya kumunda.
11 Ower. 7.25; 8.5-21 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;
mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,
12amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;
ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14Monga moto upsereza nkhalango,
ndi monga lawi liyatsa mapiri.
15Momwemo muwatsate ndi namondwe,
nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.
16 Mas. 35.4, 26 Achititseni manyazi pankhope pao;
kuti afune dzina lanu, Yehova.
17Achite manyazi, naopsedwe kosatha;
ndipo asokonezeke, naonongeke.
18Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,
ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.