1 2Maf. 20.12-19 Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nachira.
22Mbi. 32.31Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse.
3Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.
4Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona chiyani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa chuma changa, kamene ine sindinawaonetse.
5Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.
6Yer. 20.5Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babiloni; sipadzatsala kanthu, ati Yehova.
7Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni.
81Sam. 3.18Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.