1 Deut. 28.49 Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.
2Mas. 78.34Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani.
3Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola.
4Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.
5Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
6Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.
7Miy. 22.8Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.
82Maf. 17.6Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.
92Maf. 15.19Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.
10Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga.
11Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa.
12Deut. 4.6, 8Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.
13Amo. 5.22Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
14Deut. 32.18Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.