1Taonani, diso langa lachiona chonsechi;
m'khutu mwanga ndachimva ndi kuchizindikira.
2Chimene muchidziwa inu, inenso ndichidziwa;
sindikucheperani.
3Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse,
ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu.
4Koma inu ndinu opanga zabodza,
asing'anga opanda pake inu nonse.
5 Miy. 17.28 Mwenzi mutakhala chete konse,
ndiko kukadakhala nzeru zanu.
6Tamvani tsono kudzikanira kwanga,
tamverani kudzinenera kwa milomo yanga.
7Kodi munenera Mulungu mosalungama,
ndi kumnenera Iye monyenga?
8Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye?
Kodi mungamuimilire Mulungu pa mlandu?
9Nchokoma kodi kuti Iye akusanthuleni?
Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu?
10Adzakudzudzulani ndithu,
mukachita tsankho m'tseri.
11Ukulu wake sukuchititsani mantha,
ndi kuopsa kwake sikukugwerani kodi?
12Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa;
zodzikanira zanu zikunga malinga adothi.
13Khalani chete, ndilekeni, kuti ndinene,
chondifikira chifike.
14 Ower. 12.3 Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga,
ndi kupereka moyo wanga m'dzanja langa?
15 Mas. 23.4; Miy. 14.32 Angakhale andipha koma ndidzamlindira;
komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.
16Iye adzakhalanso chipulumutso changa,
pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pake.
17Mvetsetsani mau anga,
ndi kunenetsa kwanga kumveke m'makutu mwanu.
18Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga;
ndidziwa kuti adzandimasula ndili wolungama.
19Ndaniyo adzatsutsana nane?
Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga.
20Zinthu ziwiri zokha musandichitire,
pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu.
21 Mas. 39.10 Mundichotsere dzanja lanu kutali,
ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.
22Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha;
kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu.
23Mphulupulu zanga ndi zochimwa zanga ndi zingati?
Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi tchimo langa.
24 Deut. 32.20 Mubisiranji nkhope yanu,
ndi kundiyesa mdani wanu?
25 Yes. 42.3 Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka,
ndi kulondola ziputu zouma?
26Pakuti mundilembera zinthu zowawa,
ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga.
27Mulonganso mapazi anga m'zigologolo,
ndi kupenyerera mayendedwe anga onse;
mudzilembera malire mopanika mapazi anga.
28 Yob. 4.19 Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola,
ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.