MASALIMO 132 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide asamalira Kachisi ndi likasa. Lonjezano la MulunguNyimbo yokwerera.

1Yehova, kumbukirani Davide

kuzunzika kwake konse.

2 Mas. 65.1 Kuti analumbira Yehova,

nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,

3Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,

ngati ndidzakwera pa kama logonapo;

4ngati ndidzalola maso anga agone,

kapena zikope zanga ziodzere;

5 Mac. 7.46 kufikira nditapezera Yehova malo,

chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?

6Taonani, tinachimva mu Efurata;

tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango.

7Tidzalowa mokhalamo Iye;

tidzagwadira kumpando wa mapazi ake.

8 Num. 10.35 Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;

Inu ndi hema wa mphamvu yanu.

9 Yes. 61.10 Ansembe anu avale chilungamo;

ndi okondedwa anu afuule mokondwera.

10Chifukwa cha Davide mtumiki wanu

musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.

11 2Sam. 7.12 Yehova analumbira Davide zoona;

sadzalibweza; ndi kuti,

Wa iwo okhala zipatso za thupi lako

ndidzaika pa mpando wachifumu wako.

12Ana ako akasunga chipangano changa

ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa,

ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,

13 Mas. 48.1-2 pakuti Yehova anasankha Ziyoni;

analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,

14Pampumulo panga mpano posatha,

Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.

15 Mas. 147.14 Ndidzadalitsatu chakudya chake;

aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.

16Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso:

Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera.

17 1Maf. 11.36; Luk. 1.69 Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga;

ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali.

18 Mas. 35.26 Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi;

koma pa iyeyu korona wake adzamveka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help