1 Yoh. 8.32, 36; Mac. 15.10 Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
2Mac. 15.1Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu.
3Aro. 2.25Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.
4Aro. 9.31-32Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.
5Aro. 8.24-25Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.
6Agal. 3.28; Yak. 2.18, 20, 22Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.
7Agal. 3.1Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?
8Agal. 1.6Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani.
91Ako. 5.6Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse.
10Agal. 1.7Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake.
111Ako. 1.23; 15.30Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha.
12Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.
13 1Ako. 8.9; 9.19 Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
14Mat. 22.39Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
15Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane.
Ntchito za thupi ndi zipatso za Mzimu16 Aro. 8.14 Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.
17Aro. 7.23Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
18Aro. 8.14Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.
191Ako. 3.3Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,
20kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,
21Aef. 5.5njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
22Yoh. 15.2Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
23chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
24Aro. 6.6Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.
25 Aro. 8.4-5 Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.
26Afi. 2.3Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.