2 AKORINTO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau Oyamba Kalata yachiwiri ya Paulo Mtumwi yolembera kwa Akorinto inalembedwa panthawi imene ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto sunali bwino konse. Anthu ena a ku mpingo wa ku Korinto ankamunena Paulo, komabe iye anaonetsa kuti amafunitsitsa kuti ayanjane naonso ndipo izi zitachitika, iye anakondwera kwambiri.Mu gawo loyamba la kalatayi Paulo akukamba za ubale wake ndi mpingo wa ku Korinto, ndipo akulongosola chifukwa chimene iye anawayankha mokwiya potsata chipongwe chimene iwo anamuchitira komanso za mtsutsano umene unalipo mu mpingowo. Iye akulongosola kuti ali ndi chimwemwe kuti kukwiya kwake kunathandizira kuti iwo alape ndi kuyanjana. Kenaka akuwupempha mpingowo kuti upereke moolowa manja pothandiza Akhristu osowa a ku Yudeya. Mu mitu yomalizira, Paulo akuteteza utumiki wake wa utumwi kwa anthu ochepa a ku Korinto amene adadzikhazikitsa wokha ngati atumwi enieni, namanena kuti Paulo ndi mtumwi wonyenga.Za mkatimuMau oyamba 1.1-11Paulo ndi mpingo wa ku Korinto 1.12—7.16Chopereka cha Akhristu a ku Yudeya 8.1—9.15Paulo adziteteza pa udindo wake monga mtumwi 10.1—13.10Mau omaliza 13.11-14