MASALIMO 18 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide(2Sam. 22)Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova, amene ananena kwa Yehova mau a nyimbo iyi m'mene Yehova anamlanditsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo: ndipo anati,

1 2Sam. 22 Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.

2 Aheb. 2.13 Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa,

ndi Mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye;

chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

3Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika,

ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.

4Zingwe za imfa zinandizinga,

ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa.

5Zingwe za manda zindizinga,

misampha ya imfa inandifikira ine.

6M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova,

ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;

mau anga anawamva mu Kachisi mwake,

ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.

7Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi,

ndi maziko a mapiri ananjenjemera

nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.

8Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake,

ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka

nuyakitsa makala.

9Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;

ndipo pansi pa mapazi ake panali mdima bii.

10Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka;

nauluka msanga pa mapiko a mphepo.

11Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga;

mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.

12Mwa kuchezemira kunali pamaso pake makongwa anakanganuka,

matalala ndi makala amoto.

13Ndipo anagunda m'mwamba Yehova,

ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake;

matalala ndi makala amoto.

14Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa;

inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

15Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,

nafukuka maziko a dziko lapansi,

mwa kudzudzula kwanu, Yehova,

mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

16Anatuma kuchokera m'mwamba, ananditenga;

anandivuula m'madzi ambiri.

17Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,

ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;

koma Yehova anali mchirikizo wanga.

19 Mas. 31.8 Ananditulutsanso andifikitse motakasuka;

anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20 1Sam. 24.19 Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa;

anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21Pakuti ndasunga njira za Yehova,

ndipo sindinachitire choipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga,

ndipo malemba ake sindinawachotse kwa ine.

23Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye,

ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa.

24 1Sam. 26.23 Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa chilungamo changa,

monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pake.

25 1Maf. 8.32 Pa wachifundo mukhala wachifundo;

pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.

26Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;

pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27 Miy. 6.16-17 Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;

koma maso okweza muwatsitsa.

28Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;

Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;

ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30 Mas. 119.140; Miy. 30.5 Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake;

mau a Yehova ngoyengeka;

ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.

31 1Sam. 2.2; Yes. 45.5 Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?

Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'chuuno,

nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

33 2Sam. 2.18 Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala,

nandiimitsa pamsanje panga.

34Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo;

kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

35 Yes. 63.9 Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;

ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,

ndipo chifatso chanu chandikuza ine.

36Mwandipondetsa patalipatali,

sanaterereke mapazi anga.

37Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza,

ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.

38Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka,

adzagwa pansi pa mapazi anga.

39Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo;

mwandigonjetsera amene andiukira.

40Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine,

kuti ndipasule ondidawo.

41 Miy. 1.28; Yes. 1.15 Anafuula, koma panalibe wopulumutsa;

ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze.

42Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo;

ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

43 Yes. 55.5 Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;

mwandiika mutu wa amitundu;

mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.

44Pakumva m'khutu za ine adzandimvera,

alendo adzandigonjera monyenga.

45Alendo adzafota,

nadzatuluka monjenjemera m'ngaka mwao.

46Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;

nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.

47Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango,

nandigonjetsera mitundu ya anthu.

48Andipulumutsa kwa adani anga.

Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine,

mundikwatula kwa munthu wachiwawa.

49Chifukwa chake Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu,

ndipo dzina lanu ndidzaliimbira.

50 2Sam. 7.13, 29; Mas. 144.10 Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu;

nachitira chifundo wodzozedwa wake,

Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help