CHIVUMBULUTSO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBuku la Chivumbulutso lidalembedwa pa nthawi ina pamene Akhristu ankazunzidwa chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu kuti Iye ndi Ambuye. Wolemba bukuli akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu onse kuti akhale okhulupirika kwa Ambuye pamene akukumana ndi mavuto komanso mazunzo.Pafupi mau onse a m'bukuli akamba za zobisika ndi zinsinsi zina ndi zina zimene mlembiyo adazimva ndi kuziwona m'masomphenya; ndipo amazilongosola mwa njira ya mafanizo ndi mau ophiphiritsa, kotero kuti Akhristu okha pa masiku akalewo ankamvetsapo mauwo, chonsecho anzao onse akunja sankatha kutulukira tanthauzo lake lenileni. Mfundo zake za bukuli amazikamba mobwerezabwereza mwa njira zosiyanasiyana, potsata zomwe zija anaziwona m'masomphenya; motero nkwapatali kutanthauzira imodziimodzi mwa nkhani zonsezo movemerezana. Komabe phunziro lalikulu lopezeka m'bukuli nlakuti, lidzafika tsiku lina pamene, kudzera mwa Khristu Ambuye, Mulungu adzagonjetsa kotheratu adani ake onse ndi Satana yemwe; ndipo adzapereka mphotho kwa anthu ake okhulupirika, adzawadalitsa poti adzakonzanso zonse kuti zikhale zatsopano.Za mkatimuYohane apereka moni kwa mipingo isanu ndi iwiri 1.1-8Aona Khristu m'masomphenya 1.9-20Makalata olembera mipingo isanu ndi iwiri 2.1—3.22Za m'mene amapembedzera Kumwamba 4.1-11Za Mwanawankhosa ndi buku lomatidwa ndi zimatiro 5.1—8.1Za angelo asanu ndi awiri oliza malipenga 8.2—11.19Za chinjoka ndi zilombo ziwiri 12.1—13.18Zina ndi zina zooneka m'masomphenya 14.1—15.8Za mbale zisanu ndi ziwiri za ukali wa Mulungu 16.1-21Za kugwa kwa Babiloni ndi kugonjetsedwa kwa Satana 17.1—20.10Za chiweruzo chotsiriza 20.11-15Za dziko latsopano ndi Yerusalemu watsopano 21.1—22.5Mau otsiriza: za kubwera kwa Yesu 22.6-21
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help