1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi;
3Yos. 24.14ndipo anachita chigololo iwo mu Ejipito, anachita chigololo mu ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza mawere ao, pomweponso anakhudza nsonga za mawere za unamwali wao.
4Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng'ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.
5Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye;
6ovala chibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo.
7Ndipo anachita nao zigololo zake, ndiwo anthu osankhika a ku Asiriya onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.
8Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.
92Maf. 15.19; 17.3-6Chifukwa chake ndampereka m'dzanja la mabwenzi ake, m'dzanja la Aasiriya amene anawaumirira.
10Ezk. 16.37, 41Iwowa anavula umaliseche wake, anatenga ana ake aamuna ndi aakazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lake linamveka mwa akazi atamchitira maweruzo.
11Yer. 3.8-11Pamene mng'ono wake Oholiba anachiona, anavunda ndi kuumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake.
122Maf. 16.7, 10Anaumirira Aasiriya, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, ovala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika.
13Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi.
14Ndipo anaonjeza zigololo zake, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Ababiloni olembedwa ndi kundwe;
15omangira malamba m'chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonyika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.
162Maf. 24.1Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga kudziko la Ababiloni.
17Namdzera a ku Babiloni ku kama wa chikondi, namdetsa ndi chigololo chao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wake unafukidwa nao.
18M'mwemo iye anawulula chigololo chake, navula umaliseche wake; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkulu wake.
19Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m'dziko la Ejipito.
20Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya abulu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.
21Momwemo wautsanso choipa cha ubwana wako, pakukhudza Aejipito nsonga za mawere ako, chifukwa cha mawere a ubwana wako.
22 Ezk. 16.37 Chifukwa chake, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe,
23a ku Babiloni, ndi Ababiloni, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasiriya onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.
24Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.
25Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakuchitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakuchotsera ana ako aamuna ndi aakazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto.
26Adzakuvulanso zovala zako, ndi kukuchotsera zokometsera zako zokongola.
27Ezk. 16.41Motero ndidzakuleketsera choipa chako, ndi chigololo chako chochokera m'dziko la Ejipito; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Ejipito.
28Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m'dzanja la iwo amene uwada, m'dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao;
29ndipo adzachita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira ntchito, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa; ndi umaliseche wa zigololo zako udzavulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.
30Izi adzakuchitira chifukwa watsata amitundu, ndi kuchita nao chigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao.
31Wayenda m'njira ya mkulu wako, chifukwa chake ndidzapereka chikho chake m'dzanja lako.
32Atero Ambuye Yehova, M'chikho cha mkulu wako udzamweramo ndicho chachikulu ngati thumba; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo.
33Udzadzala ndi kuledzera ndi chisoni, ndi chikho chodabwitsa ndi cha chipasuko, ndi chikho cha mkulu wako Samariya.
34Mas. 75.8Udzamwa ichi ndi kugugudiza, ndi kuchechetachecheta zibade zake, ndi kung'amba mawere ako; pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova.
35Yer. 2.32; Neh. 9.26Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako.
36 Ezk. 23.4 Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Uwafotokozere tsono zonyansa zao.
37Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao aamuna amene anandibalira, kuti athedwe.
38Anandichitiranso ichi, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo, naipsa masabata anga;
392Maf. 21.4-5pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.
40Ndiponso munatuma kuitana anthu ochokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, chifukwa cha iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kuvala zokometsera;
41ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pake; pamenepo unaika chofukiza chonga ndi mafuta anga.
42Ndipo phokoso lalikulu lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao olodzera ochokera kuchipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao.
43Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzachita zigololo naye, ndi iyenso nao.
44Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wachigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo.
45Ezk. 16.38Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a achigololo, ndi maweruzo a akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo achigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi.
46Ezk. 16.40-41Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda chuma chao.
47Ndi msonkhanowo udzawaponya miyala, ndi kuwatha ndi malupanga ao, adzawapha ana ao aamuna ndi aakazi, ndi kutentha nyumba zao ndi moto.
48Momwemo ndidzaleketsa dama m'dzikomo, kuti alangizidwe akazi onse kusachita monga mwa dama lanu.
49Ezk. 23.35Ndipo adzakubwezerani dama lanu, nimudzasenza machimo a mafano anu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.