1 Afi. 3.12-14; Aheb. 9.14 Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,
2Mac. 8.14-17; 17.31-32; 19.4-5; 24.25a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.
3Lev. 4.3; 2Mbi. 26.18Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.
4Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,
5nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza,
6Eks. 28.1koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.
7Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:
8koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.
9Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;
101Ate. 1.3; Aro. 15.25; 2Ako. 8.4pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.
11Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro;
12Aheb. 10.36kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.
13 Gen. 22.16-17 Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha,
14nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.
15Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.
16Eks. 22.11Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.
17Aro. 11.29Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;
18kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;
19Aheb. 9.7chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;
20Aheb. 9.24m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.