1 MBIRI 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Adzukulu a Rubeni

1 Gen. 29.32; 48.15-22 Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.

2Gen. 49.8, 10; Mik. 5.2; Mat. 2.6Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);

3ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele: Hanoki, ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi.

4Ana a Yowele: Semaya mwana wake, Gogi mwana wake, Simei mwana wake,

5Mika mwana wake, Reaya mwana wake, Baala mwana wake,

62Maf. 15.29Beera mwana wake, amene Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.

7Ndi abale ake monga mwa mabanja ao, powerenga chibadwidwe cha mibadwo yao: akulu ndiwo Yeiyele, ndi Zekariya,

8ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni;

9ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Yufurate; pakuti zoweta zao zinachuluka m'dziko la Giliyadi.

10Ndipo masiku a Saulo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Giliyadi.

Adzukulu a Gadi

11Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m'dziko la Basani mpaka Saleka:

12Yowele mkulu wao, ndi Safamu wachiwiri, ndi Yanai, ndi Safati mu Basani;

13ndi abale ao a nyumba za makolo ao: Mikaele, ndi Mesulamu, ndi Sheba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri.

14Awa ndi ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikaele, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi,

15Ahi mwana wa Abidiyele, mwana wa Guni, ndiye mkulu wa nyumba za makolo ao.

16Ndipo anakhala mu Giliyadi mu Basani, ndi m'midzi yake, ndi podyetsa pake ponse pa Saroni, mpaka malire ao.

17Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a chibadwidwe chao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobowamu mfumu ya Israele.

18Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira chikopa ndi lupanga, ndi kuponya mivi, ozolowera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akutuluka kunkhondo.

19Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Nodabu.

202Maf. 22.4Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.

21Ndipo analanda zoweta zao, ngamira zao zikwi makumi asanu, ndi nkhosa zikwi mazana awiri ndi makumi asanu, ndi abulu zikwi ziwiri, ndi amuna zikwi zana limodzi.

222Maf. 15.29Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende.

Adzukulu a Manase kum'mawa

23Ndi anthu a hafu la fuko la Manase anakhala m'dziko; anachuluka kuyambira Basani kufikira Baala-Heremoni, ndi Seniri, ndi phiri la Heremoni.

24Ndipo akulu a nyumba za makolo ao ndi awa: Efere, ndi Isi, ndi Eliyele, ndi Aziriele, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadiyele, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.

252Maf. 17.7Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nachita chigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.

262Maf. 15.19, 29Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help