MASALIMO 105 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Alemekeza Yehova pa zodabwitsa adazichitira ana a Israele(1Mbi. 16.8-22)

1 1Mbi. 16.8-22 Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake;

bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye.

2 Mas. 77.12 Muimbireni, muimbireni zomlemekeza;

fotokozerani zodabwitsa zake zonse.

3Mudzitamandire ndi dzina lake loyera:

mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.

4 Mas. 27.8 Funani Yehova, ndi mphamvu yake;

funsirani nkhope yake nthawi zonse.

5Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita;

zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake;

6inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wake,

inu ana a Yakobo, osankhika ake.

7 Yes. 26.9 Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu;

maweruzo ake akhala padziko lonse lapansi.

8 Luk. 1.72 Akumbukira chipangano chake kosatha,

mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

9 Gen. 17.2; 26.13; 35.11-12 chipanganocho anapangana ndi Abrahamu,

ndi lumbiro lake ndi Isaki;

10ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba,

chikhale chipangano chosatha kwa Israele.

11Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,

gawo la cholowa chako;

12pokhala iwo anthu owerengeka,

inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;

13nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina,

kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena.

14 Gen. 20.3, 7; 35.5 Sanalola munthu awasautse;

ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa.

15Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga,

musamachitira choipa aneneri anga.

16 Gen. 41.54 Ndipo anaitana njala igwere dziko;

anathyola mchirikizo wonse wa mkate.

17 Gen. 37.28, 36 Anawatsogozeratu munthu;

anamgulitsa Yosefe akhale kapolo:

18 Gen. 39.20 Anapweteka miyendo yake ndi matangadza;

anamgoneka mu unyolo;

19kufikira nyengo yakuchitika maneno ake;

mau a Yehova anamuyesa.

20 Gen. 41.14 Mfumuyo anatuma munthu nammasula;

woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira.

21 Gen. 41.40 Anamuika akhale woyang'anira nyumba yake,

ndi woweruza wa pa zake zonse:

22Amange nduna zake iye mwini,

alangize akulu ake adziwe nzeru.

23 Gen. 46.6 Pamenepo Israele analowa mu Ejipito;

ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.

24 Eks. 1.7 Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake,

nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.

25 Eks. 1.8-14 Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake,

kuti achite monyenga ndi atumiki ake.

26 Eks. 3.10; 4.12, 14 Anatuma Mose mtumiki wake,

ndi Aroni amene adamsankha.

27 Eks. 7—12 Anaika pakati pao zizindikiro zake,

ndi zodabwitsa m'dziko la Hamu.

28 Eks. 10.22 Anatumiza mdima ndipo kunada;

ndipo sanapikisane nao mau ake.

29 Eks. 7.20 Anasanduliza madzi ao akhale mwazi,

naphanso nsomba zao.

30 Eks. 8.6 Dziko lao linachuluka achule,

m'zipinda zomwe za mafumu ao.

31 Eks. 8.17, 24 Ananena, ndipo inadza mitambo ya ntchentche,

ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse.

32 Eks. 9.23, 25 Anawapatsa mvula yamatalala,

lawi la moto m'dziko lao.

33Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao;

nathyola mitengo kufikira m'malire ao onse.

34 Eks. 10.4, 13-14 Ananena, ndipo linadza dzombe

ndi mphuchi, ndizo zosawerengeka,

35ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao,

zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao.

36 Eks. 12.29 Ndipo Iye anapha achisamba onse m'dziko mwao,

choyambira cha mphamvu yao yonse.

37 Eks. 12.35 Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide:

ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.

38 Eks. 12.33 Ejipito anakondwera pakuchoka iwo;

popeza kuopsa kwao kudawagwera.

39 Eks. 13.21 Anayala mtambo uwaphimbe;

ndi moto uunikire usiku.

40 Eks. 16.12-18 Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri,

nawakhutitsa mkate wakumwamba.

41 Eks. 17.6; 1Ako. 10.4 Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi;

nayenda pouma ngati mtsinje.

42 Gen. 15.13-14 Popeza anakumbukira mau ake oyera,

ndi Abrahamu mtumiki wake.

43Potero anatulutsa anthu ake ndi kusekerera,

osankhika ake ndi kufuula mokondwera.

44 Yos. 13.7 Ndipo anawapatsa maiko a amitundu;

iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:

45 Deut. 4.1, 40 Kuti asamalire malemba ake,

nasunge malamulo ake.

Aleluya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help