AHEBRI 7 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mkulu wa ansembe Melkizedeki afanizira Yesu Khristu, Mkulu wa ansembe wosatha

1 Gen. 14.18-20 Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,

2amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere;

3wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

4 Gen. 14.18-20; Num. 18.21, 26 Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.

5Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;

6Gen. 14.19; Aro. 4.13koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano.

7Ndipo popanda chitsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkulu.

8Aheb. 6.20Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo.

9Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzilimodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi;

10pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.

11 Agal. 2.21 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

12Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.

13Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

14Yes. 11.1; Luk. 3.32-33; Chiv. 5.5Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.

15Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melkizedeki,

16amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

17Mas. 110.4pakuti amchitira umboni,

Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha

monga mwa dongosolo la Melkizedeki.

18Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake,

19Mac. 13.39; Aheb. 8.6; Aef. 2.18(pakuti chilamulo sichinachitire kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.

20Ndipo monga momwe sikudachitike kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro;

21Mas. 110.4koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye,

Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa,

iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).

22 Aheb. 8.6 Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.

23Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe;

24koma Iye chifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika,

25Aro. 8.34kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.

26 Aheb. 4.15 Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;

27Lev. 9.7; 16.15; Aro. 6.10amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.

28Aheb. 5.1-2, 9Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help