2 MAFUMU 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Amaziya mfumu ya Yuda ndi Yehowasi mfumu ya Israele(2Mbi. 25.1-24)

1Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai mu Yerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.

3Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.

4Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

52Maf. 12.20Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake;

6Deut. 24.16koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.

7Anapha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.

8Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.

9Ower. 9.8-15Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama yakuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.

10Deut. 8.14; Ezk. 28.2, 5, 17Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;

112Maf. 23.29Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.

12Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake.

13Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.

141Maf. 7.51Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya.

15Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?

16Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Yerobowamu mwana wake.

17Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.

18Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?

192Mbi. 25.27Ndipo anamchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide.

21Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.

22Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.

Yerobowamu wachiwiri mfumu ya Israele

23Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.

24Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.

25Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.

262Maf. 13.4Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.

272Maf. 13.5Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.

28Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?

29Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help