MASALIMO 20 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Kupempherera mfumu potulukira iye kunkhondoKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Miy. 18.10 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso;

dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;

2likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera,

ndipo likugwirizize kuchokera mu Ziyoni;

3likumbukire zopereka zako zonse,

lilandire nsembe yako yopsereza;

4 Mas. 21.2 likupatse cha mtima wako,

ndipo likwaniritse upo wako wonse.

5 Mas. 9.14; 60.4 Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu,

ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera;

Yehova akwaniritse mapempho ako onse.

6Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake;

adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera

ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.

7 2Mbi. 32.8; Mas. 33.16-17; Miy. 21.31 Ena atama magaleta, ndi ena akavalo;

koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.

8Iwowa anagonjeka, nagwa;

koma ife tauka, ndipo takhala chilili.

9Yehova, pulumutsani,

mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help