1 TIMOTEO 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zoyenera oyang'anira ndi atumiki

1 Mac. 17.15 Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino.

2Aro. 16.21Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

3Aef. 3.13wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;

4Mac. 20.24woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.

5Tit. 1.6Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?

6Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.

7Mac. 22.12Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

8Lev. 10.9; Mac. 6.3Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;

91Tim. 1.19okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m'chikumbu mtima choona.

10Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa.

11Tit. 2.3Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.

12Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.

13Mat. 25.21Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

14Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa,

15Aef. 2.21-22kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.

16Mat. 28.2; Yoh. 1.14, 32-33; Mac. 1.9; 10.34; Akol. 1.6, 23Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help