1 Mat. 22.44; Mrk. 12.36; Luk. 20.42; Mac. 2.34; 1Ako. 15.25; Aheb. 1.13 Yehova ananena kwa Ambuye wanga,
Khalani padzanja lamanja langa,
kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
2Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni;
chitani ufumu pakati pa adani anu.
3 Ower. 5.2 Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu:
M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha,
muli nao mame a ubwana wanu.
4 Gen. 14.18; Aheb. 5.6 Yehova walumbira, ndipo sadzasintha,
Inu ndinu wansembe kosatha
monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki.
5 Mas. 2.5, 12 Ambuye padzanja lamanja lako
adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.
6Adzaweruza mwa amitundu,
adzadzaza dziko ndi mitembo;
adzaphwanya mitu m'maiko ambiri.
7 Ower. 7.5-6 Adzamwa kumtsinje wa panjira;
chifukwa chake adzaweramutsa mutu wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.