YEREMIYA 45 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau a Mulungu kwa Baruki

1 Yer. 36.4, 32 Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti,

2Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:

3Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.

4Yes. 5.5Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.

5Mas. 131.1-2; Yer. 39.18; Aro. 12.16Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help