ESTERE 10 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ukulu wa Mordekai

1Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja.

2Est. 9.4Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya?

3Gen. 41.40; Neh. 2.10; Mas. 122.8-9Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help