MIYAMBO 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Rut. 4.11 Mkazi yense wanzeru amanga banja lake;

koma wopusa alipasula ndi manja ake.

2Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;

koma wokhota m'njira yake amnyoza.

3M'kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza;

koma milomo ya anzeru idzawasunga.

4Popanda zoweta modyera muti see;

koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu.

5 Eks. 23.1 Mboni yokhulupirika siidzanama;

koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

6Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;

koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.

7Pita pamaso pa munthu wopusa,

sudzazindikira milomo yakudziwa.

8Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake;

koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.

9Zitsiru zinyoza kupalamula;

koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.

10Mtima udziwa kuwawa kwakekwake;

mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.

11 Yob. 8.15 Nyumba ya oipa idzapasuka;

koma hema wa oongoka mtima adzakula.

12 Aro. 6.21 Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;

koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.

13Ngakhale m'kuseka mtima uwawa;

ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.

14Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake;

koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.

15Wachibwana akhulupirira mau onse;

koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.

16Wanzeru amaopa nasiya zoipa;

koma wopusa amanyada osatekeseka.

17Wokangaza kukwiya adzachita utsiru;

ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.

18Achibwana amalandira cholowa cha utsiru;

koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.

19Oipa amagwadira abwino,

ndi ochimwa pa makomo a olungama.

20Waumphawi adedwa ndi anzake omwe;

koma akukonda wolemera achuluka.

21 Mas. 41.1 Wonyoza anzake achimwa;

koma wochitira osauka chifundo adala.

22Kodi oganizira zoipa sasochera?

Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.

23M'ntchito zonse muli phindu;

koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.

24Korona wa anzeru ndi chuma chao;

utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25Mboni yoona imalanditsa miyoyo;

koma wolankhula zonama angonyenga.

26Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;

ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

27Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,

kupatutsa kumisampha ya imfa.

28Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;

koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29 Yak. 1.19 Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;

koma wansontho akuza utsiru.

30Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;

koma nsanje ivunditsa mafupa.

31 Mat. 25.40, 45 Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake;

koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.

32 Mas. 23.4; 2Ako. 5.8; 2Tim. 4.18 Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake;

koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.

33Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira,

nidziwika pakati pa opusa.

34Chilungamo chikuza mtundu wa anthu;

koma tchimo lichititsa fuko manyazi.

35 Mat. 24.45, 47 Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru;

koma idzakwiyira wochititsa manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help