YOBU 14 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Gen. 7.9 Munthu wobadwa ndi mkazi

ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.

2 Mas. 90.5-9 Atuluka ngati duwa, nafota;

athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,

ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4 Mas. 51.5; Yoh. 3.6; Aro. 5.12; Aef. 2.3 Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani?

Nnena mmodzi yense.

5Popeza masiku ake alembedwa,

chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu,

ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye;

6mumleke osamthira maso, kuti apumule,

kuti akondwere nalo tsiku lake monga wolembedwa ntchito.

7Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso,

ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa.

8Ngakhale muzu wake wakalamba m'nthaka,

ndi tsinde lake likufa pansi.

9Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,

nudzaswa nthambi ngati womera.

10Koma munthu akufa atachita liondeonde

inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?

11Madzi achoka m'nyanja,

ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12 Mas. 102.26 momwemo munthu agona pansi, osaukanso;

kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,

kapena kuutsidwa pa tulo take.

13Ha? Mukadandibisa kumanda,

mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.

Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?

Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,

mpaka kwafika kusandulika kwanga.

15Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;

mukadakhumba ntchito ya manja anu.

16 Yer. 32.19 Koma tsopano muwerenga moponda mwanga;

kodi simuyang'anitsa tchimo langa?

17 Hos. 13.12 Cholakwa changa chaikidwa m'thumba lokhomedwa chizindikiro;

ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;

ndi thanthwe lisunthika m'malo mwake.

19Madzi anyenya miyala;

zosefukira zao zikokolola fumbi la nthaka;

ndipo muononga chiyembekezo cha munthu.

20Mumpambana kotheratu, napita iye;

musintha nkhope yake, mumuuza achoke.

21Ana ake aona ulemu osadziwa iye;

napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.

22Koma thupi lake limuwawira yekha,

ndi mtima wake umliritsa yekha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help