MASALIMO 117 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Alemekezedwe Mulungu pa chifundo chake
1 Aro. 15.11 Lemekezani Yehova, amitundu onse;
muimbireni, anthu onse.
2 Deut. 32.4; Mas. 100.5 Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu;
ndi choonadi cha Yehova nchosatha.
Aleluya.