MASALIMO 144 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide ayamika Mulungu kuti anamtchinjiriza, napempha ampulumutse kuti anthu adalensoSalimo la Davide.

1Wolemekezeka Yehova thanthwe langa,

wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo,

zala zanga zigwirane nao:

2 2Sam. 22.2-3, 40, 48 Ndiye chifundo changa, ndi linga langa,

msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga;

chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama;

amene andigonjetsera anthu anga.

3 Mas. 8.4; Aheb. 2.6 Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa?

Mwana wa munthu kuti mumsamalira?

4 Mas. 102.11 Munthu akunga mpweya;

masiku ake akunga mthunzi wopitirira.

5 Yes. 64.1 Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike:

Khudzani mapiri ndipo adzafuka.

6Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa;

tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa.

7 Mas. 18.16 Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba;

ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu,

kudzanja la alendo;

8amene pakamwa pao alankhula zachabe,

ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.

9 Mas. 33.2-3 Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu;

pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.

10 Mas. 18.50 Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso:

Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.

11Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo,

amene pakamwa pao alankhula zachabe,

ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo.

12 Mas. 128.3; 1Pet. 3.5 Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime;

ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya,

zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

13Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu;

ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.

14Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu;

ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo,

pasakhalenso kufuula m'makwalala athu.

15 Deut. 33.29 Odala anthu akuona zotere;

odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help