YEREMIYA 23 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau akutsutsa abusa osakhulupirika

1 Ezk. 34.2 Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova.

2Eks. 32.34Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonde; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova.

3Ezk. 34.13, 31Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka.

4Ezk. 34.23-25, 31Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.

Mphukira wa Davide

5 Yes. 4.2; Luk. 1.32-33 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.

6Zek. 14.11; 1Ako. 1.30Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.

7Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito;

8Yes. 43.5-6koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m'dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.

Mau akutsutsa aneneri onama

9Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.

10Hos. 4.2-3Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.

11Zef. 3.4Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

12Mas. 35.6Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.

13Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasocheretsa anthu anga Israele.

14Gen. 19.24; Yes. 1.9-10; Yer. 29.21-23Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.

15 Yer. 8.14 Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.

16Yer. 14.14Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

17Ezk. 13.10Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.

18Yes. 40.13-14Pakuti ndani waima mu upo wa Yehova, kuti aone namve mau ake? Ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19Yer. 30.23-24Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.

20Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino.

21Yer. 14.14Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanene ndi iwo, koma ananenera.

22Yer. 23.18Koma akadaima mu upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao.

23Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patali?

241Maf. 8.27; Mas. 139.7-12Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.

25Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26Ichi chidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a chinyengo cha mtima wao?

27Ower. 3.7Amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimtcha nalo Baala.

28Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova.

29Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?

30 Deut. 18.20-22 Chifukwa chake, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wake.

31Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene achita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.

32Zef. 3.4Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatume iwo, sindinauze iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.

33Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi chiyani? Pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.

34Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yake.

35Mudzatero yense kwa mnansi wake, ndi yense kwa mbale wake, Yehova wayankha chiyani? Ndipo Yehova wanena chiyani?

36Ndipo katundu wa Yehova simudzatchulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wake; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.

37Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanenanji?

38Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, chifukwa chake Yehova atero: Chifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova;

39Hos. 4.6chifukwa chake, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakuchotsani, ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzauchotsa pamaso panga;

40Yer. 20.11ndipo ndidzakutengerani inu chitonzo chamuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzawailika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help