1 Afi. 1.27; 2.16 Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
2 Afi. 2.2 Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.
3Luk. 10.20Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.
4 Aro. 12.12; Yak. 5.8-9 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
5Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.
6Mas. 55.22Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
7Yoh. 14.27Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
9Afi. 3.17Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Paulo ayamika Afilipi popeza adamtumiza zomthandizira10 2Ako. 11.9 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.
111Tim. 6.6, 8Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.
121Ako. 4.11Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.
13Yoh. 15.5Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.
14Afi. 1.7Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.
152Ako. 11.8-9Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;
16pakuti mu Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.
17Aro. 15.28Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.
18Afi. 2.25; Aheb. 13.16Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
19Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
20Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen.
21 Agal. 1.2 Perekani moni kwa woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni.
22Afi. 1.13Oyera mtima onse akupatsani inu moni, koma makamaka iwo a banja la Kaisara.
23Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.