1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.
3Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.
4Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu.
5Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.
6Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.
7Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.
8Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n'kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n'kubereka akatungurume.
9Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake.
10Aheb. 9.4Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
11Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza, momwemo anachita.
12Pamenepo ana a Israele ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.
13Yense wakuyandikiza chihema cha Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.