1 2Sam. 5.11-25 Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.
2Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israele; pakuti ufumu wake unakwezekadi, chifukwa cha anthu ake Israele.
3Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana aamuna ndi aakazi ena.
4Maina a ana anali nao mu Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu Natani, ndi Solomoni,
5ndi Ibara, ndi Elisuwa, ndi Elipeleti,
6ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,
7ndi Elisama, ndi Beeliyada, ndi Elifeleti.
8Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisraele onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawatulukira.
9Afilisti tsono anafika, nafalikira m'chigwa cha Refaimu.
10Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kuti, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.
11Atafika tsono ku Baala-Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.
12Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto.
13Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'chigwamo.
14Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.
15Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo utulukire kunkhondo; pakuti Mulungu watulukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.
16Nachita Davide monga Mulungu adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibiyoni kufikira ku Gezere.
17Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.