MASALIMO 126 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ayamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo waoNyimbo yokwerera.

1 Mac. 12.9 Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni,

tinakhala ngati anthu akulota.

2 Yob. 8.20-21 Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,

ndi lilime lathu linafuula mokondwera;

pamenepo anati kwa amitundu,

Yehova anawachitira iwo zazikulu.

3Yehova anatichitira ife zazikulu;

potero tikhala okondwera.

4Bwezani ukapolo wathu, Yehova,

ngati mitsinje ya kumwera.

5 Yer. 31.9-14 Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

6Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;

adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera,

alikunyamula mitolo yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help