1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng'ombe yaikazi yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m'goli;
3Aheb. 13.11-12ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.
4Aheb. 9.13Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pa chihema chokomanako.
5Pamenepo atenthe ng'ombe yaikaziyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake.
6Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yaikazi.
7Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
8Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
9Aheb. 9.13Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.
10Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.
11Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;
12iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.
13Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
14Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
15Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.
16Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
17Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m'chotengera madzi oyenda;
18ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.
19Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.
20Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.
21Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.