YESAYA 34 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yehova aipidwa ndi amitundu

1 Deut. 32.1 Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo.

2Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa.

3Yow. 2.20Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.

4Ezk. 32.7-8; Mat. 24.29; Chiv. 6.13-14Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.

5Yer. 46.10; Mala. 1.4Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.

6Yer. 49.13Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.

7Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta.

8Yes. 63.4Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu wa Ziyoni.

9Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi fumbilo lidzasanduka sulufure, ndi dziko lakelo lidzasanduka matope oyaka moto.

10Chiv. 18.18Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthawi zonse; m'mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.

11Zef. 2.14Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.

12Iwo adzaitana mfulu zake zilowe mu ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ake onse adzakhala chabe.

13Hos. 9.6Ndipo minga idzamera m'nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.

14Ndipo zilombo za m'chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde manchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

15Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake.

16Mala. 3.16Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo.

17Ndipo Iye wachita maere, chifukwa cha zilombozi, ndipo dzanja lake lazigawira dzikolo ndi chingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwomibadwo, zidzakhala m'menemo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help